19 Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Kodi Yowabu ndi amene wakutuma?”+ Mayiyo anayankha kuti: “Ndikulumbira pali moyo wanu mbuyanga mfumu, zimene inu mwanena mbuyanga nʼzoona. Mtumiki wanu Yowabu ndi amene wandituma kuti ndidzanene zonse zomwe ndalankhulazi.