32 Abisalomu anayankha kuti: “Ine ndinakutumizira uthenga wakuti, ‘Ubwere kuno ndikutume kwa mfumu ukanene kuti: “Nʼchifukwa chiyani ndinabwerako ku Gesuri?+ Zikanakhala bwino ndikanangokhala komweko. Ndikufuna ndionane ndi mfumu, ndipo ngati ndili wolakwa, mfumu indiphe.”’”