37 Ndiloleni ine mtumiki wanu ndibwerere ndikafere mumzinda wakwathu pafupi ndi manda a bambo ndi mayi anga.+ Koma mukhoza kuwoloka ndi mtumiki wanu Chimamu+ kuti mupite naye limodzi mbuyanga mfumu, ndipo mukamuchitire zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino.”