16 Zitatero asilikali amphamvuwo analimbana ndi anthu mpaka kulowa mumsasa wa Afilisiti nʼkutunga madzi mʼchitsime chimene chinali pageti la ku Betelehemu ndipo anapita nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa madziwo. Mʼmalomwake anawapereka kwa Yehova powathira pansi.+