21 Arauna anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti: “Ndabwera kudzagula malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe, kuti mliri umene uli pakati pa anthuwu uthe.”+