13 Mupite kwa Mfumu Davide mukanene kuti, ‘Kodi si inu mbuyanga mfumu amene munalumbirira ine kapolo wanu kuti: “Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo panga, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu”?+ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya wakhala mfumu?’