42 Mfumuyo itamva zimenezi inaitanitsa Simeyi nʼkumufunsa kuti: “Kodi sindinakulumbiritse pamaso pa Yehova nʼkukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluke nʼkupita kwina kulikonse, udziwiretu kuti udzafaʼ? Ndipo kodi iwe sunandiuze kuti, ‘Mwanena bwino. Ndichita zimene mwanenaziʼ?+