66 Tsiku lotsatira, Solomo anauza anthuwo kuti azipita, ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo nʼkumapita kwawo. Anapita akusangalala, ali ndi chimwemwe mumtima chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake komanso anthu ake Aisiraeli.