21 Rehobowamu atangofika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa asilikali ophunzitsidwa bwino okwana 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini. Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi nyumba ya Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu mwana wa Solomo.+