4 Mfumu Yerobowamu atangomva mawu otemberera guwa lansembe la ku Beteli amene munthu wa Mulunguyo ananena, anasiya zimene ankachita paguwa lansembe nʼkumuloza ndipo ananena kuti: “Mʼgwireni uyu!”+ Nthawi yomweyo, dzanja limene analozera munthu wa Mulunguyo linauma ndipo sanathe kulibweza.+