6 Mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde, pemphani Yehova Mulungu wanu kuti andichitire chifundo ndipo mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woonayo anapempha Yehova kuti achitire chifundo mfumuyo, moti dzanjalo linabwerera mwakale.