-
1 Mafumu 15:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Zitatero, Asa anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi pa chuma chamʼnyumba ya mfumu nʼkumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa anatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene ankakhala ku Damasiko. Anawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti:
-