26 Mfumu ya Asuri inauzidwa kuti: “Mitundu imene munaichotsa kwawo nʼkukaiika mʼmizinda ya ku Samariya sikudziwa chipembedzo cha Mulungu wa kumeneko. Choncho iye wakhala akuwatumizira mikango imene ikuwapha chifukwa palibe amene akudziwa chipembedzo cha Mulungu wa kumeneko.”