19 chifukwa chakuti mtima wako unali womvera ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova.