2 Ndiyeno mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova pamodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu onse okhala ku Yerusalemu, ansembe, aneneri ndi anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inayamba kuwawerengera mawu onse amʼbuku+ la pangano+ limene linapezeka mʼnyumba ya Yehova.+