3 Mfumuyo inaima pafupi ndi chipilala ndipo inachita pangano pamaso pa Yehova,+ kuti idzatsatira Yehova ndiponso kusunga malamulo ake ndi zikumbutso zake. Idzachita zimenezi ndi mtima wonse ndi moyo wonse potsatira mawu a pangano olembedwa mʼbukulo. Ndipo anthu onsewo anavomereza panganolo.+