12 Mfumuyo inagumulanso maguwa ansembe amene mafumu a Yuda anamanga padenga+ la chipinda chapamwamba cha Ahazi. Inagumulanso maguwa ansembe amene Manase anamanga pamabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ Kenako inawaperapera ndipo fumbi lake inakaliwaza kuchigwa cha Kidironi.