30 Choncho atumiki ake ananyamula mtembo wake pagaleta kuchokera ku Megido nʼkupita nawo ku Yerusalemu ndipo anakamuika mʼmanda ake. Kenako anthu amʼdzikolo anatenga Yehoahazi mwana wa Yosiya nʼkumudzoza ndiponso kumuveka ufumu mʼmalo mwa bambo ake.+