13 Ndiyeno Elisa anauza Gehazi kuti: “Muuze kuti, ‘Mwavutika ndi kutisamalira,+ kodi tingakuchitireni chiyani?+ Kodi pali chinachake choti tikakunenereni kwa mfumu,+ kapena kwa mkulu wa asilikali?’” Koma mayiyo anayankha kuti: “Ayi, palibe. Ndikukhala mwamtendere ndi anthu a mtundu wanga.”