7 Mfumu ya Isiraeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu kuti ndili ndi mphamvu zoti ndingaphe munthu kapena kumusiya wamoyo?+ Wanditumizira munthu uyu nʼkundiuza kuti ndimuchiritse khate. Mukhoza kuona nokha kuti akufuna kuyambana nane.”