15 Zitatero iye ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona uja.+ Atafika ananena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu koma ku Isiraeli.+ Chonde landirani mphatso iyi kuchokera kwa ine mtumiki wanu.”