6 Yehova anali atachititsa asilikali a mumsasa wa Asiriyawo kumva phokoso la magaleta ankhondo, phokoso la mahatchi ndi phokoso la gulu lalikulu la asilikali.+ Choncho anthuwo anauzana kuti: “Anthuni! Mfumu ya Isiraeli yaitanitsa mafumu a Ahiti ndi mafumu a Iguputo kuti adzamenyane nafe!”