16 Zitatero, anthu anapita kukatenga zinthu mumsasa wa Asiriya. Choncho ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake unafika pa sekeli imodzi ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake unafikanso pa sekeli imodzi, mogwirizana ndi mawu a Yehova.+