-
2 Mafumu 10:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehu atachoka pamenepo, anakumana ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu+ amene anabwera kudzakumana naye. Atamupatsa moni,* anamʼfunsa kuti: “Kodi mtima wako wonse uli ndi ine ngati mmene mtima wanga ulili ndi mtima wako?”
Yehonadabu anayankha kuti: “Inde.”
Ndiyeno Yehu anati: “Ngati ndi choncho ndipatse dzanja lako.”
Choncho Yehonadabu anapereka dzanja lake ndipo Yehu anamukweza mʼgaleta lake.
-