17 Kenako Elisa anati: “Tsegulani windo lakumʼmawa.” Iye analitsegula. Ndiyeno Elisa anati: “Ponyani muviwo!” Choncho iye anauponya. Zitatero Elisa anati: “Muvi wa Yehova wopulumutsa! Muvi wopulumutsa kwa Asiriya! Mudzapha Asiriya ku Afeki+ mpaka kuwamaliza.”