25 Kenako Peka+ mwana wa Remaliya, yemwe anali msilikali wake womʼthandiza pagaleta, anamʼkonzera chiwembu nʼkumupha ku Samariya. Iye anapha mfumuyo ali limodzi ndi Arigobi, Ariye ndiponso amuna 50 a ku Giliyadi. Anaiphera munsanja ya panyumba ya mfumu, nʼkuyamba kulamulira mʼmalo mwake.