13 Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse ndiponso amasomphenya onse+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo muzisunga malamulo anga, mogwirizana ndi malamulo onse amene ndinalamula makolo anu ndiponso amene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”