41 Anthu omwe atchulidwa mayinawa, anapita kumeneko pa nthawi imene Hezekiya+ anali mfumu ya Yuda ndipo anagwetsa mahema a mbadwa za Hamu komanso anapha Ameyuni amene anali kumeneko. Anapha anthuwa ndipo iwo kulibe mpaka lero. Kenako anayamba kukhala kumeneko, chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo.