28 Cholowa chawo ndiponso malo awo okhala anali Beteli+ ndi midzi yake yozungulira. Kumʼmawa kunali Naarani, kumadzulo kunali Gezeri ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Sekemu ndi midzi yake yozungulira mpaka kukafika ku Aya ndi midzi yake yozungulira.