2 Kenako Davide anatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu. Anapeza kuti chinali cholemera talente imodzi ya golide ndipo chinali chokongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali. Anthu anaveka Davide chipewacho. Komanso iye anatenga zinthu zambiri mumzindawo.+