3 Davide anatenga anthu amene anali mumzindawo nʼkuyamba kuwagwiritsa ntchito+ yocheka miyala komanso ntchito zina zogwiritsa ntchito zitsulo zakuthwa ndi nkhwangwa. Zimenezi ndi zimene anachitira anthu onse amʼmizinda ya Aamoni. Kenako Davide ndi asilikali onse anabwerera ku Yerusalemu.