-
1 Mbiri 21:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Komanso Mulungu woona anatumiza mngelo ku Yerusalemu kuti akawononge mzindawo. Koma mngeloyo atangotsala pangʼono kuyamba kuwononga, Yehova anaona zimenezo ndipo anamva chisoni chifukwa cha mliriwo,+ choncho anauza mngelo amene ankawonongayo kuti: “Basi!+ Bweza dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehovayo anali ataima pafupi ndi malo opunthira mbewu a Orinani+ wa Chiyebusi.+
-