19 Choncho muzifunafuna Yehova Mulungu wanu+ ndi mtima wanu wonse ndiponso moyo wanu wonse. Yambani kumanga nyumba yopatulika ya Yehova Mulungu woona,+ kuti mukatenge likasa la pangano la Yehova ndi ziwiya zopatulika za Mulungu woona+ nʼkuziika mʼnyumba ya dzina la Yehova imene imangidweyo.”+