16 Mfumu Asa inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu, chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri lolambirira mzati wopatulika.+ Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera nʼkukalitentha mʼchigwa cha Kidironi.+