2 Patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ngʼombe zambiri nʼkuzipereka nsembe mʼmalo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+