11 Komanso Uziya anali ndi gulu la asilikali okonzeka kumenya nkhondo. Iwo ankapita kunkhondo mʼmagulumagulu. Asilikaliwa anawerengedwa komanso kulembedwa mayina+ ndi Yeyeli mlembi+ ndiponso Maaseya womuthandiza wake. Awiriwa ankayangʼaniridwa ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu.