21 Mfumu Uziya anakhala wakhate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye ankakhala mʼnyumba yayekha chifukwa cha khatelo+ popeza anali atamuchotsa mʼnyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndi amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu komanso kuweruza anthu amʼdzikolo.+