22 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya analankhula ndi Alevi onse amene ankachita zinthu mwanzeru potumikira Yehova ndiponso anawalimbikitsa. Anthuwo anachita phwando kwa masiku 7.+ Ankapereka nsembe zamgwirizano+ komanso kuthokoza Yehova Mulungu wa makolo awo.