31 Mfumuyo inaimirira pamalo ake ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo ake ndiponso zikumbutso zake. Inanena kuti idzachita zimenezi ndi mtima wake wonse+ ndi moyo wake wonse potsatira mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.+