3 Ndiyeno anauza Alevi, alangizi a Aisiraeli onse,+ omwe anali oyera kwa Yehova, kuti: “Ikani Likasa lopatulika mʼnyumba imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli anamanga.+ Musamalinyamulenso pamapewa anu.+ Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisiraeli.