25 Yeremiya+ anaimba nyimbo ya maliro a Yosiya. Oimba onse aamuna ndi aakazi+ amaimba zokhudza Yosiya akamaimba nyimbo za maliro mpaka lero. Panakhazikitsidwa lamulo loti nyimbo zimenezi ziziimbidwa mu Isiraeli ndipo zinaikidwa mʼgulu la nyimbo zoimba pamaliro.