8 Ndaikanso lamulo lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akuluakulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa ndalama zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho kuti ntchitoyo isaime.+