-
Ezara 9:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo, koma watisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse nʼcholinga choti tikamangenso nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anawonongedwa, ndiponso kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.*
-