6 Kenako Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona nʼkupita kuchipinda chodyera cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye chakudya kapena kumwa madzi, popeza ankalira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.+