8 Kenako Uziyeli mwana wa Harihaya, mmodzi wa osula golide, anakonza mpandawo kuchokera pamene analekezera. Hananiya mmodzi wa opanga mafuta onunkhira, anapitiriza kuchokera pamene Uziyeli analekezera. Iwo anayala miyala mu Yerusalemu mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+