-
Nehemiya 5:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Komanso ndinakutumula zovala zanga nʼkunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Mulungu woona akutumule munthu amene sachita zimene walonjeza nʼkumuchotsa mʼnyumba yake ndi pa zinthu zake zonse. Akutumulidwe chonchi nʼkukhala wopanda kanthu.” Ndiyeno gulu lonse la anthulo linati: “Ame!”* Anthuwo anatamanda Yehova ndipo anachita zimene analonjezazo.
-