6 Mʼkalatayo analembamo kuti: “Pali mphekesera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ Nʼchifukwa chake ukumanga mpandawo ndipo mogwirizana ndi zimene anthu akunenazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo.