36 Tizibweretsanso ana athu aamuna oyamba kubadwa ndiponso a ziweto zathu+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo. Tizibweretsa ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi nkhosa zathu. Tizibweretsa zimenezi kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene amatumikira mʼnyumba ya Mulungu wathu.+