5 Eliyasibu anapatsa Tobia chipinda chachikulu chosungira katundu. Poyamba mʼchipindachi ankaikamo nsembe yambewu, lubani, ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda apageti ankayenera kulandira, komanso zimene ankapereka kwa ansembe.+