-
Esitere 2:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Anthuwo asonkhanitse anamwali okongola kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndipo azikhala mʼnyumba ya akazi. Atsikanawa aziyangʼaniridwa ndi Hegai,+ munthu wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa.
-